-
Mateyu 18:8, 9Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
8 Choncho ngati dzanja lako kapena phazi lako limakupunthwitsa, ulidule nʼkulitaya kutali.+ Ndi bwino kuti ukapeze moyo ulibe chiwalo chimodzi kapena uli wolumala kusiyana nʼkuti uponyedwe mʼmoto wosatha uli ndi manja onse awiri kapena mapazi onse awiri.+ 9 Komanso ngati diso lako limakuchimwitsa* ulikolowole nʼkulitaya kutali. Ndi bwino kuti ukapeze moyo uli ndi diso limodzi kusiyana nʼkuti uponyedwe mu Gehena* wamoto uli ndi maso onse awiri.+
-