-
Luka 4:5-8Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
5 Choncho anapita naye pamalo okwera ndipo anamuonetsa maufumu onse apadziko lapansi mʼkanthawi kochepa.+ 6 Ndiyeno Mdyerekezi anamuuza kuti: “Ndikupatsani ulamuliro pa maufumu onsewa ndi ulemerero wawo wonse, chifukwa unaperekedwa kwa ine+ ndipo ndikhoza kuupereka kwa aliyense amene ndingakonde kumupatsa. 7 Ndiye ngati inuyo mungandilambire kamodzi kokha, ulamuliro wonsewu udzakhala wanu.” 8 Poyankha Yesu anamuuza kuti: “Malemba amati, ‘Yehova* Mulungu wako ndi amene uyenera kumulambira ndipo uyenera kutumikira iye yekha basi.’”+
-