23 Pa nthawiyo, mʼsunagoge mwawomo munali munthu wogwidwa ndi mzimu wonyansa, ndipo munthuyo anafuula kuti: 24 “Kodi mukufuna chiyani kwa ife, inu Yesu Mnazareti?+ Kodi mwabwera kudzatiwononga? Inetu ndikukudziwani bwino kwambiri, ndinu Woyera wa Mulungu!”+