-
Mateyu 4:5-7Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
5 Kenako Mdyerekezi anamutenga nʼkupita naye mumzinda woyera,+ ndipo anamukweza pamwamba pa khoma la mpanda wa kachisi*+ 6 nʼkumuuza kuti: “Ngati ndinu mwana wa Mulungu mudziponye pansi, paja Malemba amati: ‘Iye adzalamula angelo ake zokhudza inu,’ komanso amati, ‘Adzakunyamulani mʼmanja mwawo, kuti phazi lanu lisawombe mwala.’”+ 7 Koma Yesu anamuyankha kuti: “Malemba amanenanso kuti: ‘Yehova* Mulungu wanu musamamuyese.’”+
-