46 Ndiyeno Mariya ananena kuti: “Moyo wanga ukulemekeza Yehova,+ 47 ndipo mzimu wanga sungalephere kusefukira ndi chimwemwe mwa Mulungu, Mpulumutsi wanga,+ 48 chifukwa waona malo otsika a kapolo wake wamkazi.+ Ndipo taonani! kuyambira tsopano mibadwo yonse idzanditcha wosangalala.+