-
Mateyu 23:25, 26Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
25 Tsoka kwa inu alembi ndi Afarisi, anthu achinyengo inu! Chifukwa muli ngati kapu ndi mbale zimene zatsukidwa kunja kokha+ koma mkati mwake muli mwakuda. Mkati mwa mitima yanu mwadzaza dyera*+ ndi kusadziletsa.+ 26 Mfarisi wakhungu iwe, yeretsa mkati mwa kapu ndi mbale choyamba, kuti kunja kwakenso kukhale koyera.
-