-
Mateyu 23:27, 28Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
27 Tsoka kwa inu alembi ndi Afarisi, anthu achinyengo inu!+ Chifukwa mumafanana ndi manda opaka laimu,+ amene kunja kwake amaonekadi okongola, koma mkati mwake muli mafupa a anthu akufa ndi zonyansa zamitundu yonse. 28 Mofanana ndi zimenezi, pamaso pa anthu, inunso mumaoneka ngati olungama koma mkati mwanu mwadzaza chinyengo ndi kusamvera malamulo.+
-