32 Choncho aliyense amene akuvomereza pamaso pa anthu kuti ndi wophunzira wanga,+ inenso ndidzamuvomereza pamaso pa Atate wanga wakumwamba kuti ndi wophunzira wanga.+ 33 Koma aliyense amene adzandikane pamaso pa anthu, inenso ndidzamukana pamaso pa Atate wanga wakumwamba.+