-
Salimo 49:16-19Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
16 Musachite mantha chifukwa chakuti munthu wina walemera,
Kapena chifukwa chakuti katundu wamʼnyumba mwake wawonjezeka,
17 Chifukwa akadzamwalira sadzatenga china chilichonse.+
Ulemerero wake sadzapita nawo limodzi.+
18 Chifukwa pamene anali moyo ankatamanda moyo wake.+
(Anthu amakutamanda ukalemera.)+
19 Koma pamapeto pake amafa ngati mmene makolo ake anachitira.
Iwo sadzaonanso kuwala.
-