16 Iwo ankauza mapiri ndi matanthwe kuti: “Tigwereni,+ tibiseni kuti tisaonekere kwa Mulungu amene wakhala pampando wachifumu+ ndiponso kuti mkwiyo wa Mwanawankhosa usatigwere,+ 17 chifukwa tsiku lalikulu la mkwiyo wawo lafika,+ ndipo ndi ndani amene angaimirire pamaso pawo?”+