-
Yohane 12:28-30Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
28 Atate lemekezani dzina lanu.” Atatero mawu+ anamveka kuchokera kumwamba kuti: “Ndalilemekeza ndipo ndidzalilemekezanso.”+
29 Choncho gulu la anthu amene anali ataimirira pamenepo anamva zimenezi ndipo anayamba kunena kuti kwagunda bingu. Ena ankanena kuti: “Mngelo walankhula naye.” 30 Yesu anawauza kuti: “Mawu amenewa sanamveke chifukwa cha ine, koma chifukwa cha inu.
-
-
1 Yohane 5:9Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
9 Nʼzoona kuti timakhulupirira umboni umene anthu amapereka, komatu umboni umene Mulungu amapereka ndi woposa umboni umenewo. Choncho timakhulupirira umboni umene Mulungu amapereka wokhudza Mwana wake.
-