Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Machitidwe 8:32
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 32 Mawu a mʼMalemba amene ankawerengawo anali akuti: “Anamutengera kumalo oti akamuphere ngati nkhosa. Ndipo mofanana ndi mwana wa nkhosa amene wangokhala chete pamene akufuna kumumeta ubweya, sanatsegule pakamwa pake.+

  • Machitidwe 8:35
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 35 Zitatero, Filipo anayamba kumuuza uthenga wabwino wonena za Yesu, ndipo anayambira palemba lomweli.

  • 1 Petulo 1:18, 19
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 18 Mukudziwa inu kuti zinthu zimene zinakumasulani*+ ku moyo wanu wopanda phindu umene munatengera kuchokera kwa makolo anu, sizinali zinthu zotha kuwonongeka monga siliva kapena golide. 19 Koma munamasulidwa ndi magazi amtengo wapatali+ a Khristu,+ omwe ndi ofanana ndi magazi a nkhosa yopanda chilema komanso yopanda mawanga.+

  • Chivumbulutso 5:6
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 6 Kenako ndinaona mwana wa nkhosa+ amene ankaoneka ngati waphedwa,+ ataimirira pakati pa mpando wachifumu ndi angelo 4 aja komanso pakati pa akulu aja.+ Iye anali ndi nyanga 7 ndiponso maso 7. Maso amenewa akuimira mizimu 7 ya Mulungu,+ imene yatumizidwa padziko lonse lapansi.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena