19 “Anthu anu amene anafa adzakhalanso ndi moyo.
Anthu anga amene anafa adzadzuka nʼkuimirira.+
Dzukani ndipo mufuule mosangalala,
Inu anthu okhala mʼfumbi!+
Chifukwa mame anu ali ngati mame amʼmawa,
Ndipo dziko lapansi lidzatulutsa anthu amene anafa kuti akhalenso ndi moyo.