Yohane 14:16 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 16 Ine ndidzapempha Atate ndipo adzakupatsani mthandizi* wina kuti adzakhale nanu mpaka kalekale.+ Yohane 14:26 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 26 Koma mthandizi, amene ndi mzimu woyera umene Atate wanga adzatumize mʼdzina langa, adzakuphunzitsani komanso kukukumbutsani zinthu zonse zimene ndinakuuzani.+ Yohane 15:26 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 26 Akadzafika mthandizi amene ndidzakutumizireni kuchokera kwa Atate, amene ndi mzimu wa choonadi+ wochokera kwa Atate, ameneyo adzandichitira umboni,+ Machitidwe 2:32, 33 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 32 Yesu ameneyo Mulungu anamuukitsa, ndipo tonsefe ndife mboni za nkhani imeneyi.+ 33 Iye anakwezedwa nʼkukhala kudzanja lamanja la Mulungu+ ndipo analandira mzimu woyera wolonjezedwawo kuchokera kwa Atate.+ Choncho iye watipatsa* mzimu woyera umene mukuuona ndi kuumvawu.
26 Koma mthandizi, amene ndi mzimu woyera umene Atate wanga adzatumize mʼdzina langa, adzakuphunzitsani komanso kukukumbutsani zinthu zonse zimene ndinakuuzani.+
26 Akadzafika mthandizi amene ndidzakutumizireni kuchokera kwa Atate, amene ndi mzimu wa choonadi+ wochokera kwa Atate, ameneyo adzandichitira umboni,+
32 Yesu ameneyo Mulungu anamuukitsa, ndipo tonsefe ndife mboni za nkhani imeneyi.+ 33 Iye anakwezedwa nʼkukhala kudzanja lamanja la Mulungu+ ndipo analandira mzimu woyera wolonjezedwawo kuchokera kwa Atate.+ Choncho iye watipatsa* mzimu woyera umene mukuuona ndi kuumvawu.