-
Levitiko 23:5-7Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
5 Mʼmwezi woyamba, pa tsiku la 14 la mweziwo,+ madzulo kuli kachisisira,* lizikhala tsiku la Pasika wa Yehova.+
6 Pa tsiku la 15 la mwezi umenewu, muzichitira Yehova Chikondwerero cha Mikate Yopanda Zofufumitsa.+ Muzidya mikate yopanda zofufumitsa kwa masiku 7.+ 7 Pa tsiku loyamba la chikondwererocho muzichita msonkhano wopatulika+ ndipo musamagwire ntchito iliyonse yotopetsa.
-