-
Machitidwe 6:8Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
8 Sitefano anali ndi mphamvu ndipo ankachita kuonekeratu kuti Mulungu ali naye. Iye ankachita zinthu zodabwitsa ndi zizindikiro zazikulu pakati pa anthu.
-
-
Machitidwe 15:12Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
12 Zitatero gulu lonselo linakhala chete, ndipo linayamba kumvetsera pamene Baranaba ndi Paulo ankafotokoza zizindikiro ndi zodabwitsa zambiri zimene Mulungu anachita pakati pa anthu a mitundu ina kudzera mwa iwo.
-
-
Aroma 15:18, 19Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
18 Sindidzalankhula chilichonse chimene ndachita pandekha, koma zokhazo zimene Khristu wachita ndi kulankhula kudzera mwa ine kuti ndithandize anthu a mitundu ina kukhala omvera. 19 Iwo akhala omvera chifukwa cha zodabwitsa zamphamvu ndiponso zizindikiro+ zimene mzimu wa Mulungu wachita. Choncho ndalalikira mokwanira uthenga wabwino wonena za Khristu kuyambira ku Yerusalemu mpaka ku Iluriko.+
-