Genesis 17:9, 10 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 9 Mulungu anapitiriza kuuza Abulahamu kuti: “Koma iwe usunge pangano langa, iwe ndi mbadwa zako mʼmibadwo yawo yonse. 10 Ili ndi pangano la pakati pa ine ndi iwe, lakuti iwe ndi mbadwa zako muzilisunga: Mwamuna aliyense pakati panu azidulidwa.+ Ekisodo 12:48 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 48 Ngati mlendo amene akukhala nanu akufuna kuchita nawo chikondwerero cha Pasika kwa Yehova, mwamuna aliyense wamʼnyumba yake adulidwe. Akatero angathe kubwera kudzachita nawo chikondwererocho, ndipo ayenera kuonedwa ngati mbadwa ya dzikolo. Koma munthu wosadulidwa asadye nawo.+ Levitiko 12:2, 3 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 2 “Uza Aisiraeli kuti, ‘Mkazi akakhala woyembekezera nʼkubereka mwana wamwamuna, azikhala wodetsedwa kwa masiku 7. Azikhala wodetsedwa ngati mmene amakhalira pa nthawi imene akusamba.+ 3 Pa tsiku la 8, mwanayo azidulidwa.+
9 Mulungu anapitiriza kuuza Abulahamu kuti: “Koma iwe usunge pangano langa, iwe ndi mbadwa zako mʼmibadwo yawo yonse. 10 Ili ndi pangano la pakati pa ine ndi iwe, lakuti iwe ndi mbadwa zako muzilisunga: Mwamuna aliyense pakati panu azidulidwa.+
48 Ngati mlendo amene akukhala nanu akufuna kuchita nawo chikondwerero cha Pasika kwa Yehova, mwamuna aliyense wamʼnyumba yake adulidwe. Akatero angathe kubwera kudzachita nawo chikondwererocho, ndipo ayenera kuonedwa ngati mbadwa ya dzikolo. Koma munthu wosadulidwa asadye nawo.+
2 “Uza Aisiraeli kuti, ‘Mkazi akakhala woyembekezera nʼkubereka mwana wamwamuna, azikhala wodetsedwa kwa masiku 7. Azikhala wodetsedwa ngati mmene amakhalira pa nthawi imene akusamba.+ 3 Pa tsiku la 8, mwanayo azidulidwa.+