-
Luka 2:21, 22Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
21 Patatha masiku 8, nthawi yoti achite mdulidwe wa mwanayo itakwana,+ anamupatsa dzina lakuti Yesu. Limeneli ndi dzina limene mngelo uja anatchula Mariya asanakhale woyembekezera.+
22 Komanso nthawi yoti iwo ayeretsedwe mogwirizana ndi Chilamulo cha Mose itakwana,+ anapita ndi mwanayo ku Yerusalemu kukamupereka kwa Yehova.*
-