Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Machitidwe 19:22
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 22 Choncho ku Makedoniya anatumizako awiri mwa anthu amene ankamutumikira, omwe ndi Timoteyo+ ndi Erasito.+ Koma iye anakhalabe mʼchigawo cha Asia kwa kanthawi ndithu.

  • Aroma 16:21
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 21 Wantchito mnzanga Timoteyo akupereka moni, chimodzimodzinso Lukiyo, Yasoni ndi Sosipato omwe ndi achibale anga.+

  • 1 Akorinto 4:17
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 17 Nʼchifukwa chake ndikukutumizirani Timoteyo, popeza iye ndi mwana wanga wokondedwa ndiponso wokhulupirika mwa Ambuye. Iye adzakukumbutsani mmene ndimachitira zinthu potumikira Khristu Yesu+ komanso mmene ndimaphunzitsira kulikonse, mumpingo uliwonse.

  • 1 Atesalonika 3:2
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 2 Ndiye tinatumiza Timoteyo+ mʼbale wathu, yemwe ndi mtumiki wa Mulungu* amene akulengeza uthenga wabwino wonena za Khristu. Tinamutumiza kuti adzakulimbikitseni ndi kukutonthozani nʼcholinga choti chikhulupiriro chanu chikhale cholimba.

  • 1 Timoteyo 1:2
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 2 Ndikukulembera iwe Timoteyo,*+ mwana wanga weniweni+ mʼchikhulupiriro:

      Mulungu Atate wathu ndi Khristu Yesu Ambuye wathu akupatse kukoma mtima kwakukulu, chifundo ndi mtendere.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena