-
Aroma 8:3, 4Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
3 Chilamulo chinalibe mphamvu yokumasulani+ chifukwa anthu ndi ofooka+ komanso ochimwa. Koma kuti akumasuleni, Mulungu anatumiza Mwana wake+ ali ndi thupi ngati la anthu ochimwa+ kuti athane ndi uchimo. Choncho Mulungu anagonjetsa uchimo pogwiritsa ntchito thupi. 4 Mulungu anachita izi kuti ife amene timayenda motsatira mzimu, osati motsatira zofuna za thupi,+ tikwaniritse zinthu zolungama zimene Chilamulo chimafuna.+
-