-
Akolose 1:21, 22Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
21 Ndithudi, inu amene kale munali otalikirana ndi Mulungu ndiponso adani ake chifukwa maganizo anu anali pa ntchito zoipa, 22 tsopano wagwirizana nanunso kudzera mu imfa ya mwana wake amene anapereka thupi lake lanyama nʼcholinga choti akuperekeni pamaso pa Mulunguyo, muli opatulika ndi opanda chilema ndiponso opanda chifukwa chokunenezerani.+
-