-
Aefeso 2:15, 16Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
15 Ndi thupi lake, anathetsa chinthu choyambitsa chidani, chomwe ndi Chilamulo chimene chinali ndi malamulo komanso malangizo. Anachithetsa kuti magulu awiri omwe ndi ogwirizana ndi iye, akhale munthu mmodzi watsopano+ komanso kuti akhazikitse mtendere. 16 Ndiponso kuti kudzera mwa mtengo wozunzikirapo,*+ agwirizanitse magulu awiri a anthuwo kwa Mulungu ndipo anthuwo akhale thupi limodzi, chifukwa anali atapheratu chidanicho+ kudzera mu imfa yake.
-
-
Akolose 1:19, 20Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
19 Zili choncho chifukwa chakuti Mulungu zinamusangalatsa kuti makhalidwe ake onse akhale mwa Khristu.+ 20 Komanso kuti kudzera mwa mwana wakeyo agwirizanitsenso zinthu zina zonse+ ndi iyeyo, kaya zinthuzo ndi zapadziko lapansi kapena zakumwamba. Anachita zimenezi pokhazikitsa mtendere kudzera mʼmagazi+ amene Khristu anakhetsa pamtengo wozunzikirapo.*
-