-
Aefeso 3:5, 6Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
5 Mʼmibadwo yamʼmbuyo, chinsinsi chimenechi sichinaululidwe kwa ana a anthu mmene Mulungu wachiululira panopa kwa atumwi ndi aneneri ake oyera kudzera mwa mzimu.+ 6 Chinsinsi chimenechi nʼchakuti anthu a mitundu ina amene ndi ogwirizana ndi Khristu Yesu, adzalandire cholowa chimene Khristu adzalandire, ndipo adzakhala mbali ya thupi.+ Iwo adzalandiranso zinthu zimene Mulungu watilonjeza chifukwa cha uthenga wabwino.
-
-
Akolose 2:2Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
2 Ndikuchita zimenezi kuti mitima yawo ilimbikitsidwe+ ndiponso kuti onse akhale ogwirizana mʼchikondi+ komanso kuti alandire chuma chonse chimene chimabwera chifukwa chomvetsa bwino zinthu, popanda kukayikira chilichonse, nʼcholinga choti adziwe molondola chinsinsi chopatulika cha Mulungu, chomwe ndi Khristu.+
-