2 Mayina a atumwi 12 ndi awa:+ Simoni, amene ankatchulidwa kuti Petulo*+ ndi Andireya+ mchimwene wake. Yakobo mwana wa Zebedayo ndi mchimwene wake Yohane.+
33 Pa ola lomwelo ananyamuka nʼkubwerera ku Yerusalemu. Kumeneko anakapeza ophunzira 11 aja komanso anthu ena amene anasonkhana nawo pamodzi. 34 Iwo anawauza kuti: “Nʼzoonadi, Ambuye auka kwa akufa ndipo aonekera kwa Simoni!”+