-
Aroma 7:12, 13Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
12 Choncho Chilamulo pachokha nʼchoyera ndipo malamulo ndi oyera, olungama ndiponso abwino.+
13 Kodi zimenezi zikutanthauza kuti chinthu chabwino chinachititsa kuti ndife? Ayi. Uchimo ndi umene unachititsa kuti ndife. Chilamulo nʼchabwino, kungoti chinachititsa kuti zidziwike bwino kuti uchimo ukuchititsa kuti ndife.+ Choncho malamulo anatithandiza kudziwa kuti uchimo ndi woipa kwambiri.+
-