9 Ndithudi abale, mukukumbukira kuti tinayesetsa kugwira ntchito mwakhama ndi mphamvu zathu zonse. Tinkagwira ntchito usiku ndi masana kuti aliyense wa inu asatilipirire kanthu kalikonse pofuna kutithandiza,+ pamene tinkalalikira uthenga wabwino wa Mulungu kwa inu.