-
Malaki 3:10Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
10 Bweretsani gawo limodzi pa magawo 10 alionse* a zinthu zanu nʼkuziika mosungiramo zinthu zanga,+ kuti mʼnyumba mwanga mukhale chakudya.+ Ndiyeseni chonde pa nkhani imeneyi, kuti muone ngati sindidzakutsegulirani mageti akumwamba+ nʼkukukhuthulirani madalitso mpaka simudzasowa kanthu,”+ watero Yehova wa magulu ankhondo akumwamba.
-
-
Afilipi 4:18, 19Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
18 Komabe, ine ndili ndi zonse zimene ndikufunikira ndipo zikuposa pa zimene ndikufunikira. Sindikusowa kanthu chifukwa Epafurodito+ wandipatsa zinthu zimene mwanditumizira. Zinthu zimenezi zili ngati fungo lonunkhira bwino+ ndiponso nsembe yovomerezeka yomwe ndi yosangalatsa kwa Mulungu. 19 Chifukwa cha zimenezi, Mulungu wanga adzakupatsani zonse zimene mukufunikira+ mogwirizana ndi kuchuluka kwa chuma chake chaulemerero, kudzera mwa Khristu Yesu.
-