3 Sitikuchita chilichonse chokhumudwitsa, kuti anthu asapezere chifukwa utumiki wathu.+ 4 Koma tikusonyeza mʼnjira iliyonse kuti ndife atumiki a Mulungu.+ Tikuchita zimenezi popirira zinthu zambiri, pokumana ndi mavuto, pokhala opanda zinthu zofunika, pokumana ndi zinthu zovuta,+