8 Kukoma mtima kwakukulu kumeneku kunaperekedwa kwa ine, munthu wamngʼono pondiyerekeza ndi wamngʼono kwambiri pa oyera onse.+ Ndinapatsidwa kukoma mtima kumeneku+ kuti ndilengeze kwa anthu a mitundu ina uthenga wabwino wonena za chuma chopanda polekezera cha Khristu,