-
1 Petulo 4:1, 2Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
4 Popeza Khristu anavutika pa nthawi imene anali munthu,+ nanunso konzekerani pokhala ndi maganizo ofanana ndi amene Khristu anali nawo. Zili choncho chifukwa munthu amene akuvutika ndiye kuti anasiya kuchita machimo.+ 2 Anachita zimenezi kuti pa nthawi yonse imene ali moyo asamachite zofuna za anthu+ koma za Mulungu.+
-