Ekisodo 20:12 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 12 Muzilemekeza bambo anu ndi mayi anu+ kuti mukhale ndi moyo nthawi yaitali mʼdziko limene Yehova Mulungu wanu akukupatsani.+ Deuteronomo 5:16 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 16 Muzilemekeza bambo anu ndi mayi anu+ mogwirizana ndi zimene Yehova Mulungu wanu anakulamulani, kuti mukhale ndi moyo nthawi yaitali komanso kuti zinthu zikuyendereni bwino mʼdziko limene Yehova Mulungu wanu akukupatsani.+ Miyambo 20:20 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 20 Aliyense amene amatemberera bambo ake komanso mayi ake,Nyale yake idzazimitsidwa kukagwa mdima.+ Miyambo 23:22 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 22 Uzimvera bambo ako amene anakubereka,Ndipo usanyoze mayi ako chifukwa chakuti akalamba.+ Mateyu 15:4 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 4 Mwachitsanzo, Mulungu ananena kuti, ‘Muzilemekeza bambo anu ndi mayi anu.’+ Komanso anati, ‘Aliyense wolankhula mawu achipongwe kwa bambo ake kapena mayi ake aziphedwa.’+
12 Muzilemekeza bambo anu ndi mayi anu+ kuti mukhale ndi moyo nthawi yaitali mʼdziko limene Yehova Mulungu wanu akukupatsani.+
16 Muzilemekeza bambo anu ndi mayi anu+ mogwirizana ndi zimene Yehova Mulungu wanu anakulamulani, kuti mukhale ndi moyo nthawi yaitali komanso kuti zinthu zikuyendereni bwino mʼdziko limene Yehova Mulungu wanu akukupatsani.+
4 Mwachitsanzo, Mulungu ananena kuti, ‘Muzilemekeza bambo anu ndi mayi anu.’+ Komanso anati, ‘Aliyense wolankhula mawu achipongwe kwa bambo ake kapena mayi ake aziphedwa.’+