-
1 Akorinto 9:16, 17Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
16 Ngati ndikulalikira uthenga wabwino, chimenecho si chifukwa chodzitamira, chifukwa ndinalamulidwa kuchita zimenezi. Tsoka kwa ine ngati sindilalikira uthenga wabwino.+ 17 Ndikamachita zimenezi mwa kufuna kwanga, ndidzalandira mphoto. Koma ngakhale nditachita mokakamizika, ndinebe woyangʼanira mogwirizana ndi udindo umene ndinapatsidwa.+
-
-
Akolose 1:25, 26Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
25 Ndinakhala mtumiki wa mpingo umenewu mogwirizana ndi udindo+ umene Mulungu anandipatsa woti ndilalikire mawu a Mulungu mokwanira, kuti inuyo mupindule. 26 Mawuwo akuphatikizapo chinsinsi chopatulika+ chimene dziko silinachidziwe+ ndiponso chinali chobisika kwa mibadwo yakale. Koma tsopano chaululidwa kwa oyera ake.+
-