-
Akolose 1:25-27Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
25 Ndinakhala mtumiki wa mpingo umenewu mogwirizana ndi udindo+ umene Mulungu anandipatsa woti ndilalikire mawu a Mulungu mokwanira, kuti inuyo mupindule. 26 Mawuwo akuphatikizapo chinsinsi chopatulika+ chimene dziko silinachidziwe+ ndiponso chinali chobisika kwa mibadwo yakale. Koma tsopano chaululidwa kwa oyera ake.+ 27 Mulungu zinamusangalatsa kuululira oyera pakati pa anthu a mitundu ina chinsinsi chopatulikachi,+ chomwe chili ndi ulemerero wochuluka komanso chuma chauzimu. Chinsinsi chimenechi ndi Khristu amene ndi wogwirizana ndi inuyo, kutanthauza kuti muli ndi chiyembekezo chodzalandira ulemerero limodzi ndi Khristuyo.+
-