4 Pa ulendowu anali limodzi ndi Sopaturo mwana wa Puro wa ku Bereya, Arisitako+ ndi Sekundo a ku Tesalonika, Gayo wa ku Debe ndi Timoteyo,+ koma ochokera mʼchigawo cha Asia anali Tukiko+ ndi Terofimo.+
2 Ku Adiramutiyo tinakwera ngalawa imene inali itatsala pangʼono kunyamuka ulendo wopita kumadoko amʼmbali mwa nyanja mʼchigawo cha Asia. Kenako tinanyamuka limodzi ndi Arisitako,+ yemwe anali wa ku Makedoniya ku Tesalonika.