19 ndi kutinso mudziwe kukula kwa mphamvu zake zopambana zimene wazisonyeza kwa okhulupirirafe.+ Mphamvu zake zazikuluzo zikuonekera muntchito zake, 20 pamene anazigwiritsa ntchito poukitsa Khristu kwa akufa nʼkumukhazika kudzanja lake lamanja+ mʼmalo akumwamba.