-
Aefeso 2:14, 15Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
14 Chifukwa iye amene anaphatikiza magulu awiri aja kukhala gulu limodzi+ nʼkugwetsa khoma lomwe linkawalekanitsa limene linali pakati pawo,+ watibweretsera mtendere.+ 15 Ndi thupi lake, anathetsa chinthu choyambitsa chidani, chomwe ndi Chilamulo chimene chinali ndi malamulo komanso malangizo. Anachithetsa kuti magulu awiri omwe ndi ogwirizana ndi iye, akhale munthu mmodzi watsopano+ komanso kuti akhazikitse mtendere.
-