2 Timoteyo 1:13 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 13 Gwiritsitsabe chitsanzo cha mawu olondola+ amene unawamva kwa ine pamene ukusonyeza chikhulupiriro ndi chikondi zomwe timakhala nazo chifukwa chogwirizana ndi Khristu Yesu. Tito 1:7 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 7 Popeza ndi mtumiki* wa Mulungu, woyangʼanira ayenera kukhala wopanda chifukwa chomunenezera. Asakhale womva zake zokha,+ wa mtima wapachala,+ womwa mowa mwauchidakwa, wankhanza* kapena wokonda kupeza phindu mwachinyengo. Tito 1:9 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 9 Akhalenso wogwira mwamphamvu mawu okhulupirika pamene akuphunzitsa mwaluso,+ kuti athe kulimbikitsa anthu ndi mfundo zolondola+ ndiponso kudzudzula+ otsutsa.
13 Gwiritsitsabe chitsanzo cha mawu olondola+ amene unawamva kwa ine pamene ukusonyeza chikhulupiriro ndi chikondi zomwe timakhala nazo chifukwa chogwirizana ndi Khristu Yesu.
7 Popeza ndi mtumiki* wa Mulungu, woyangʼanira ayenera kukhala wopanda chifukwa chomunenezera. Asakhale womva zake zokha,+ wa mtima wapachala,+ womwa mowa mwauchidakwa, wankhanza* kapena wokonda kupeza phindu mwachinyengo.
9 Akhalenso wogwira mwamphamvu mawu okhulupirika pamene akuphunzitsa mwaluso,+ kuti athe kulimbikitsa anthu ndi mfundo zolondola+ ndiponso kudzudzula+ otsutsa.