Miyambo 15:1 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 15 Kuyankha modekha* kumabweza mkwiyo,+Koma mawu opweteka amayambitsa mkwiyo.+ Mateyu 5:5 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 5 Osangalala ndi anthu ofatsa+ chifukwa adzalandira dziko lapansi.+ Agalatiya 5:22, 23 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 22 Koma makhalidwe amene anthu amakhala nawo mothandizidwa ndi mzimu woyera* ndi chikondi, chimwemwe, mtendere, kuleza mtima, kukoma mtima, ubwino,+ chikhulupiriro, 23 kufatsa ndi kudziletsa.+ Palibe lamulo loletsa makhalidwe amenewa. Akolose 3:12 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 12 Choncho monga anthu osankhidwa ndi Mulungu,+ oyera ndi okondedwa, valani chifundo chachikulu,+ kukoma mtima, kudzichepetsa,+ kufatsa+ komanso kuleza mtima.+ 1 Petulo 3:15 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 15 Koma muvomereze mumtima mwanu kuti Khristu ndi Ambuye ndiponso kuti ndi woyera. Nthawi zonse muzikhala okonzeka kuyankha aliyense amene wakufunsani za chiyembekezo chanu, koma muziwayankha mofatsa+ ndiponso mwaulemu kwambiri.+
22 Koma makhalidwe amene anthu amakhala nawo mothandizidwa ndi mzimu woyera* ndi chikondi, chimwemwe, mtendere, kuleza mtima, kukoma mtima, ubwino,+ chikhulupiriro, 23 kufatsa ndi kudziletsa.+ Palibe lamulo loletsa makhalidwe amenewa.
12 Choncho monga anthu osankhidwa ndi Mulungu,+ oyera ndi okondedwa, valani chifundo chachikulu,+ kukoma mtima, kudzichepetsa,+ kufatsa+ komanso kuleza mtima.+
15 Koma muvomereze mumtima mwanu kuti Khristu ndi Ambuye ndiponso kuti ndi woyera. Nthawi zonse muzikhala okonzeka kuyankha aliyense amene wakufunsani za chiyembekezo chanu, koma muziwayankha mofatsa+ ndiponso mwaulemu kwambiri.+