-
Machitidwe 9:1, 2Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
9 Koma Saulo anapitiriza kuopseza ophunzira a Ambuye+ komanso ankafunitsitsa kuwapha. Choncho anapita kwa mkulu wa ansembe 2 kukapempha makalata a chilolezo kuti apite nawo kumasunagoge a ku Damasiko. Anapempha makalatawo kuti akakapeza wina aliyense wotsatira Njirayo,*+ mwamuna kapena mkazi, akamumange nʼkubwera naye ku Yerusalemu.
-