-
Machitidwe 26:10, 11Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
10 Ndipo izi ndi zimene ndinachitadi ku Yerusalemu. Ndinkatsekera mʼndende oyera ambiri+ nditapatsidwa mphamvu ndi ansembe aakulu.+ Akaweruzidwa kuti aphedwe, ine ndinkavomereza. 11 Nthawi zambiri ndinkawapatsa chilango mʼmasunagoge onse, pofuna kuwakakamiza kuti asiye zimene amakhulupirira. Popeza ndinali nditakwiya nawo kwambiri, ndinafika powazunza ngakhale mʼmizinda yakunja.
-
-
1 Timoteyo 1:12, 13Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
12 Ndikuthokoza Khristu Yesu Ambuye wathu, amene anandipatsa mphamvu nʼkundipatsanso utumiki chifukwa anaona kuti ndine wokhulupirika.+ 13 Anatero ngakhale kuti kale ndinali wonyoza Mulungu, wozunza anthu ake ndiponso wachipongwe.+ Komabe anandichitira chifundo chifukwa ndinkachita zinthu mosadziwa komanso ndinalibe chikhulupiriro.
-