Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Machitidwe 9:1, 2
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 9 Koma Saulo anapitiriza kuopseza ophunzira a Ambuye+ komanso ankafunitsitsa kuwapha. Choncho anapita kwa mkulu wa ansembe 2 kukapempha makalata a chilolezo kuti apite nawo kumasunagoge a ku Damasiko. Anapempha makalatawo kuti akakapeza wina aliyense wotsatira Njirayo,*+ mwamuna kapena mkazi, akamumange nʼkubwera naye ku Yerusalemu.

  • Machitidwe 22:4
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 4 Ndinkazunza otsatira Njira imeneyi mpaka kuwapha. Ndinkamanga amuna ndi akazi nʼkukawapereka kundende.+

  • Machitidwe 26:10
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 10 Ndipo izi ndi zimene ndinachitadi ku Yerusalemu. Ndinkatsekera mʼndende oyera ambiri+ nditapatsidwa mphamvu ndi ansembe aakulu.+ Akaweruzidwa kuti aphedwe, ine ndinkavomereza.

  • Agalatiya 1:13
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 13 Munamva ndithu zimene ndinkachita ndili mʼChiyuda,+ kuti ndinkazunza kwambiri mpingo wa Mulungu ndipo ndinapitiriza kuuwononga.+

  • Afilipi 3:5, 6
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 5 ndinadulidwa pa tsiku la 8,+ ndine wa mtundu wa Isiraeli, wa fuko la Benjamini, ndine Mheberi wobadwa kwa Aheberi.+ Kunena za chilamulo, ndine Mfarisi.+ 6 Kunena za kudzipereka, ndinkazunza mpingo.+ Kunena zochita chilungamo potsatira chilamulo, ndinasonyeza kuti ndilibe chifukwa chondinenezera.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena