-
Afilipi 1:7Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
7 Nʼzoyenera kwa ine kuti ndiganizire nonsenu mwa njira imeneyi, chifukwa ndinu apamtima panga. Inu amene munandithandiza pa nthawi imene ndinamangidwa maunyolo mʼndende+ komanso poteteza uthenga wabwino ndi kukhazikitsa mwalamulo ntchito yolengeza uthenga wabwino.+ Inu limodzi ndi ine tinapindula ndi kukoma mtima kwakukulu kwa Mulungu.
-