-
Machitidwe 20:22, 23Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
22 Ndipo tsopano, motsogoleredwa ndi mzimu, ndikupita ku Yerusalemu ngakhale kuti sindikudziwa zimene zikandichitikire kumeneko. 23 Koma chinthu chimodzi chokha chimene ndikudziwa nʼchakuti mumzinda ndi mzinda, mzimu woyera wandichitira umboni mobwerezabwereza kuti ndikuyembekezera kumangidwa komanso kuzunzidwa.+
-
-
2 Akorinto 11:23-28Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
23 Kapena kodi iwo ndi atumiki a Khristu? Ndikuyankha ngati wamisala, ineyo ndiye mtumiki wa Khristu woposa iwowo. Ndachita zambiri kuposa iwowo,+ ndinamangidwa kambirimbiri,+ ndinamenyedwa kosawerengeka ndipo ndinabwererapo lokumbakumba kambirimbiri.+ 24 Maulendo 5 Ayuda anandikwapula zikwapu 40, kuchotsera chimodzi.+ 25 Katatu anandimenya ndi ndodo.+ Kamodzi anandiponya miyala.+ Ngalawa inandiswekerapo katatu.+ Kamodzi ndinakhala panyanja usiku ndi masana wonse. 26 Ndinayenda maulendo ambirimbiri, ndinakumana ndi zoopsa mʼmitsinje komanso ndinakumana ndi achifwamba pamsewu. Ndinakumananso ndi zoopsa kuchokera kwa anthu a mtundu wanga,+ anthu a mitundu ina,+ mumzinda,+ mʼchipululu, panyanja ndi pakati pa abale achinyengo. 27 Ndinkagwira ntchito zowawa komanso zotulutsa thukuta. Nthawi zambiri usiku sindinkagona,+ ndinkakhala ndi njala ndiponso ludzu+ ndipo nthawi zambiri ndinkakhala osadya,+ ndinkazizidwa komanso ndinalibe zovala zokwanira.*
28 Kuwonjezera pa zinthu zimenezi, palinso chinthu china chomwe panopa chimandivutitsa maganizo tsiku ndi tsiku. Ndimadera nkhawa mipingo yonse.+
-