-
Aroma 5:15Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
15 Koma mmene zilili ndi mphatsoyi, si mmene zinalili ndi uchimowo. Anthu ambiri anafa chifukwa cha uchimo wa munthu mmodzi. Koma kukoma mtima kwakukulu kwa Mulungu ndiponso mphatso yake yaulere imene anaipereka mokoma mtima kudzera mwa munthu mmodzi,+ Yesu Khristu, nʼzapamwamba kwambiri. Pogwiritsa ntchito mphatso imeneyi, Mulungu adzapereka madalitso osaneneka kwa anthu ambiri.+
-