34 ndani adzawatsutsa? Khristu Yesu ndi amene anafa komanso ndi amene anaukitsidwa. Iye ali kudzanja lamanja la Mulungu,+ ndipo amatilankhulira mochonderera.+
24 Khristu sanalowe mʼmalo oyera opangidwa ndi manja a anthu,+ amene ndi chithunzi cha malo enieniwo,+ koma analowa kumwamba kwenikweniko.+ Panopa iye ali kumwamba kuti azionekera pamaso pa Mulungu mʼmalo mwa ifeyo.+
2Ana anga okondedwa, ndikukulemberani zinthu izi kuti musachite tchimo. Komabe, wina akachita tchimo, tili ndi wotithandiza wolungama,+ Yesu Khristu,+ amene ali ndi Atate.