-
Aroma 5:15Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
15 Koma mmene zilili ndi mphatsoyi, si mmene zinalili ndi uchimowo. Anthu ambiri anafa chifukwa cha uchimo wa munthu mmodzi. Koma kukoma mtima kwakukulu kwa Mulungu ndiponso mphatso yake yaulere imene anaipereka mokoma mtima kudzera mwa munthu mmodzi,+ Yesu Khristu, nʼzapamwamba kwambiri. Pogwiritsa ntchito mphatso imeneyi, Mulungu adzapereka madalitso osaneneka kwa anthu ambiri.+
-
-
2 Timoteyo 1:9, 10Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
9 Iye anatipulumutsa ndiponso anatiitana kuti tikhale oyera,+ osati chifukwa cha ntchito zathu, koma chifukwa cha cholinga chake ndi kukoma mtima kwake kwakukulu.+ Mulungu anatisonyeza kukoma mtimaku kalekale chifukwa cha Khristu Yesu. 10 Koma tsopano izi zatsimikizirika chifukwa cha kuonekera kwa Mpulumutsi wathu Khristu Yesu,+ amene wathetsa mphamvu za imfa.+ Komanso pogwiritsa ntchito uthenga wabwino,+ watidziwitsa mmene tingapezere moyo+ wosawonongeka.+
-