5 Chifukwa pali Mulungu mmodzi+ ndiponso mkhalapakati mmodzi+ pakati pa Mulungu ndi anthu.+ Mkhalapakatiyu ndi Khristu Yesu,+ munthu 6 amene anadzipereka kuti akhale dipo la anthu onse lokwanira ndendende.+ Zimenezi ndi zimene zidzachitiridwe umboni pa nthawi yake.