9 Pa chifukwa chimenechi, Mulungu anamukweza nʼkumupatsa udindo wapamwamba+ ndipo mokoma mtima anamupatsa dzina loposa lina lililonse.+ 10 Anachita zimenezi kuti mʼdzina la Yesu, onse apinde mawondo awo, kaya ali kumwamba, padziko lapansi kapena pansi pa nthaka.+