6 Nsembe zanyama komanso nsembe zina, simunazifune.+
Koma munatsegula makutu anga kuti ndimve.+
Simunapemphe nsembe zopsereza ndi nsembe zamachimo.+
7 Ndiyeno ine ndinati: “Taonani, ine ndabwera.
Mumpukutu munalembedwa za ine.+
8 Ndimasangalala kuchita zimene mumafuna, inu Mulungu wanga,+
Ndipo chilamulo chanu chili mumtima mwanga.+