4 Ndimaganiza kuti, munthu ndi ndani kuti muzimuganizira,
Ndipo mwana wa munthu ndi ndani kuti muzimusamalira?+
5 Munamutsitsa pangʼono poyerekeza ndi angelo,
Ndipo munamuveka ulemerero ndi ulemu ngati chisoti chachifumu.
6 Munamupatsa mphamvu kuti alamulire ntchito za manja anu.+
Mwaika zinthu zonse pansi pa mapazi ake: